Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 119:98 - Buku Lopatulika

98 Malamulo anu andipatsa nzeru yakuposa adani anga; pakuti akhala nane chikhalire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

98 Malamulo anu andipatsa nzeru yakuposa adani anga; pakuti akhala nane chikhalire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

98 Malamulo anu amandisandutsa wanzeru kuposa adani anga, popeza kuti malamulowo ndili nawo nthaŵi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

98 Malamulo anu amachititsa kuti ndikhale wanzeru kuposa adani anga, popeza malamulowo ali ndi ine nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 119:98
12 Mawu Ofanana  

Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.


Ndinasankha njira yokhulupirika; ndinaika maweruzo anu pamaso panga.


Pakuti Yehova apatsa nzeru; kudziwa ndi kuzindikira kutuluka m'kamwa mwake.


Oipa samvetsetsa chiweruzo; koma omwe afuna Yehova amvetsetsa zonse.


Chifukwa chake asungeni, achiteni; pakuti ichi ndi nzeru zanu ndi chidziwitso chanu pamaso pa mitundu ya anthu akumva malemba ndi kuti, Ndithu mtundu waukulu uwu, ndiwo athu anzeru ndi akuzindikira.


Ndipo mtundu waukulu wa anthu ndi uti, wakukhala nao malemba ndi maweruzo olungama, akunga chilamulo ichi chonse ndichiika pamaso panu lero lino?


Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.


Koma iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m'kuchita kwake.


Ndipo Davide anakhala wochenjera m'mayendedwe ake onse; ndipo Yehova anali naye.


Pomwepo mafumu a Afilisti anatuluka; ndipo nthawi zonse anatuluka iwo, Davide anali wochenjera koposa anyamata onse a Saulo, chomwecho dzina lake linatamidwa kwambiri.


Ndipo Davide anatuluka kunka kulikonse Saulo anamtumako, nakhala wochenjera; ndipo Saulo anamuika akhale woyang'anira anthu a nkhondo; ndipo ichi chinakomera anthu onse, ndi anyamata a Saulo omwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa