Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 119:149 - Buku Lopatulika

149 Imvani liu langa monga mwa chifundo chanu; mundipatse moyo monga mwa kuweruza kwanu, Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

149 Imvani liu langa monga mwa chifundo chanu; mundipatse moyo monga mwa kuweruza kwanu, Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

149 Imvani liwu langa chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. Inu Chauta, sungani moyo wanga chifukwa cha chilungamo chanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

149 Imvani mawu anga molingana ndi chikondi chanu chosasinthika; Yehova sungani moyo wanga, molingana ndi malamulo anu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 119:149
12 Mawu Ofanana  

Koma Inu, Yehova Ambuye, muchite nane chifukwa cha dzina lanu; ndilanditseni popeza chifundo chanu ndi chabwino.


Mundinenere mlandu wanga, nimundiombole; mundipatse moyo monga mwa mau anu.


Zachifundo zanu ndi zazikulu, Yehova; mundipatse moyo monga mwa maweruzo anu.


Moyo wanga umamatika ndi fumbi; mundipatse moyo monga mwa mau anu.


Taonani, ndinalira malangizo anu; mundipatse moyo mwa chilungamo chanu.


Mundipatse moyo monga mwa chifundo chanu; ndipo ndidzasamalira mboni ya pakamwa panu.


Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zanu zokoma mufafanize machimo anga.


Mverani, ndipo mundiyankhe, ndiliralira m'kudandaula kwanga ndi kubuula;


Imvani Mulungu, mau anga, m'kudandaula kwanga; sungani moyo wanga angandiopse mdani.


Mundiyankhe Yehova; pakuti chifundo chanu nchokoma; munditembenukire monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu.


Ndidzatchula zachifundo chake cha Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wake waukulu kwa banja la Israele, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa chifundo chake, ndi monga mwa ntchito zochuluka za chikondi chake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa