Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 109:27 - Buku Lopatulika

27 kuti adziwe kuti ichi ndi dzanja lanu; kuti Inu Yehova munachichita.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 kuti adziwe kuti ichi ndi dzanja lanu; kuti Inu Yehova munachichita.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Adani adziŵe kuti limeneli ndi dzanja lanu londipulumutsa, Inu Chauta, ndinu amene mwachita zimenezi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Adaniwo adziwe kuti limeneli ndi dzanja lanu, kuti Inu Yehova mwachita zimenezi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 109:27
12 Mawu Ofanana  

Ezara amene anakwera kuchokera ku Babiloni, ndiye mlembi waluntha m'chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israele adachipereka; ndipo mfumu inampatsa chopempha iye chonse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wake.


Ndipo kunali atachimva adani athu onse, amitundu onse akutizinga anaopa, nagwadi nkhope; popeza anazindikira kuti ntchitoyi inachitika ndi Mulungu wathu.


Atsekereza mokhomera chizindikiro dzanja la munthu aliyense, kuti anthu onse anawalenga adziwe.


Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka, ndi lilime lathu linafuula mokondwera; pamenepo anati kwa amitundu, Yehova anawachitira iwo zazikulu.


Pamenepo alembi anati kwa Farao, Chala cha Mulungu ichi; koma mtima wa Farao unalimba, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.


kuti, Tidzawachitira chiyani anthu awa? Pakutitu chaoneka kwa onse akukhala mu Yerusalemu kuti chizindikiro chozindikirika chachitidwa ndi iwo, ndipo sitingathe kukana.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa