Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 103:20 - Buku Lopatulika

20 Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Tamandani Chauta, inu angelo ake, inu amphamvu amene mumamva mau ake, amene mumachita zimene amalamula.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Tamandani Yehova, inu angelo ake, amphamvu inu amene mumachita zimene amalamula, amene mumamvera mawu ake.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 103:20
14 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, usiku womwewo mthenga wa Yehova anatuluka, nakantha m'misasa ya Aasiriya zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu, ndipo pouka anthu mamawa, taonani, onsewo ndi mitembo.


Mlemekezeni, angelo ake onse; mlemekezeni, makamu ake onse.


Alemekeze dzina la Yehova; popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.


Perekani kwa Yehova, inu ana a amphamvu, perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.


Yense anadya mkate wa angelo, anawatumizira chakudya chofikira.


Pamwamba pa Iye panaima aserafi; yense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi; awiri anaphimba nao nkhope yake, awiri naphimba nao mapazi ake, awiri nauluka nao.


Ndipo ine, chaka choyamba cha Dariusi Mmedi, ndinauka kumlimbikitsa ndi kumkhazikitsa.


ndipo Yehova amveketsa mau ake pamaso pa khamu lake la nkhondo; pakuti a m'chigono mwake ndi ambirimbiri; pakuti Iye wakuchita mau ake ndiye wamphamvu ndithu; pakuti tsiku la Yehova ndi lalikulu ndi loopsa ndithu; akhoza kupirira nalo ndani?


Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi awiri?


Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.


Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Ine ndine Gabriele, woimirira pamaso pa Mulungu; ndipo ndinatumidwa kwa iwe kudzalankhula nawe, ndi kuuza iwe uthenga uwu wabwino.


Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa