Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 103:15 - Buku Lopatulika

15 Koma munthu, masiku ake akunga udzu; aphuka monga duwa lakuthengo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Koma munthu, masiku ake akunga udzu; aphuka monga duwa la kuthengo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Kunena za munthu, masiku ake sakhalitsa, ali ngati a udzu, munthuyo amakondwa ngati duŵa lakuthengo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Kunena za munthu, masiku ake ali ngati udzu, amaphuka ngati duwa la mʼmunda;

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 103:15
9 Mawu Ofanana  

Tsoka kwa korona wakunyada wa oledzera a Efuremu, ndi kwa duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu paiwo, amene agwidwa ndi vinyo, m'chigwa cha nthaka yabwino.


ndi duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu pa chigwa cha nthaka yabwino, lidzakhala ngati nkhuyu yoyamba kucha malimwe asanafike; poiona wakupenya imeneyo, amaidya ili m'dzanja lake.


Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;


Adzudzula nyanja, naiphwetsa, naumitsa mitsinje yonse; Basani ndi Karimele afota, ndi duwa la ku Lebanoni linyala.


Popeza, Anthu onse akunga udzu, ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu. Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa