Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 9:47 - Buku Lopatulika

47 Ndipo ngati diso lako likulakwitsa ulikolowole; kulowa iwe mu Ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa mu Gehena;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

47 Ndipo ngati diso lako likulakwitsa ulikolowole; kulowa iwe m'Ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa m'Gehena;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

47 “Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole. Ndi bwino kuti ukaloŵe mu Ufumu wa Mulungu uli ndi diso limodzi lokha, kupambana kuti akakuponye ku Gehena uli ndi maso onse aŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

47 Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi, kusiyana ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa mu gehena,

Onani mutuwo Koperani




Marko 9:47
14 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso, mtengo wolakalakika wopatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene anali naye, nadya iyenso.


Ndinapangana ndi maso anga, potero ndipenyerenji namwali?


Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe, mundipatse moyo mu njira yanu.


Ndipo ngati diso lako likukhumudwitsa, ulikolowole, nulitaye: nkwabwino kuti ulowe m'moyo ndi diso limodzi koposa kuponyedwa mu Gehena wamoto, uli ndi maso awiri.


koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.


Ndipo ngati dzanja lako likulakwitsa iwe, ulidule: nkwabwino kwa iwe kulowa m'moyo wopunduka dzanja, koposa kukhala ndi manja ako awiri ndi kulowa mu Gehena, m'moto wosazima.


Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sangathe kukhala wophunzira wanga.


Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sangathe kuona Ufumu wa Mulungu.


Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sangathe kulowa ufumu wa Mulungu.


Pamenepo thamo lanu lili kuti? Pakuti ndikuchitirani inu umboni, kuti, kukadatheka, mukadakolowola maso anu ndi kundipatsa ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa