Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 9:32 - Buku Lopatulika

32 Koma iwo sanazindikire mauwo, naopa kumfunsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Koma iwo sanazindikire mauwo, naopa kumfunsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Ophunzira ake sadamvetse mau ameneŵa, komabe ankaopa kumufunsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Koma sanazindikire chimene amatanthauza, ndipo anachita mantha kuti amufunse.

Onani mutuwo Koperani




Marko 9:32
12 Mawu Ofanana  

Ndipo chitatha icho anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pachakudya; ndipo anawadzudzula chifukwa cha kusavomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanavomereze iwo amene adamuona, atauka Iye.


Ndipo ananena nao, Mutero inunso opanda nzeru kodi? Kodi simuzindikira kuti kanthu kalikonse kochokera kunja kukalowa mwa munthu, sikangathe kumdetsa iye;


Koma Iye anapotoloka, napenya ophunzira ake, namdzudzula Petro, nanena, Choka, pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; popeza susamalira zinthu za Mulungu, koma za anthu.


Ndipo anasunga mauwo, nafunsana mwa iwo okha, kuti, Kuuka kwa akufa nchiyani?


Ndipo sanadziwitse kanthu ka izi; ndi mau awa adawabisikira, ndipo sanazindikire zonenedwazo.


Ndipo sanadziwitse mau amene Iye analankhula nao.


Ndipo anawatsegulira mitima yao, kuti adziwitse malembo;


Koma iwo sanadziwitse mau awa, ndipo anabisidwa kwa iwo, kuti asawadziwe; ndipo anaopa kumfunsa za mau awa.


Izi sanazidziwe ophunzira ake poyamba; koma pamene Yesu analemekezedwa, pamenepo anakumbukira kuti izi zinalembedwa za Iye, ndi kuti adamchitira Iye izi.


Yesu anazindikira kuti analikufuna kumfunsa Iye, ndipo anati kwa iwo, Kodi mulikufunsana wina ndi mnzake za ichi, kuti ndinati, Kanthawi ndipo simundiona Ine, ndiponso kanthawi nimudzandiona Ine?


Ndipo pamenepo anadza ophunzira ake; nazizwa kuti analinkulankhula ndi mkazi; koma panalibe wina anati, Mufuna chiyani? Kapena, mulankhula naye chiyani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa