Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 9:31 - Buku Lopatulika

31 Pakuti anaphunzitsa ophunzira ake, nanena nao, kuti, Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja anthu, ndipo adzamupha Iye; ndipo ataphedwa, adzauka pofika masiku atatu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Pakuti anaphunzitsa ophunzira ake, nanena nao, kuti, Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja anthu, ndipo adzamupha Iye; ndipo ataphedwa, adzauka pofika masiku atatu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 chifukwa ankaphunzitsa ophunzira ake. Ankaŵauza kuti, “Mwana wa Munthu akudzaperekedwa kwa anthu, ndipo iwowo adzamupha. Koma atamupha, Iye adzauka patapita masiku atatu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 chifukwa amaphunzitsa ophunzira ake. Anati kwa iwo, “Mwana wa Munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu. Adzamupha, ndipo patatha masiku atatu adzauka.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 9:31
19 Mawu Ofanana  

Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.


monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.


Mudziwa kuti akapita masiku awiri, Paska afika, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kupachikidwa pamtanda.


nanena, Mfumu, takumbukira ife kuti wonyenga uja anati, pamene anali ndi moyo, Ndidzauka pofika masiku atatu.


ndipo adzamnyoza Iye, nadzamthira malovu, nadzamkwapula Iye, nadzamupha; ndipo pofika masiku atatu adzauka.


Ndipo anayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kuti Mwana wa Munthu akamve zowawa zambiri, nakakanidwe ndi akulu ndi ansembe aakulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo mkucha wake akauke.


Ndipo Iye ananena nao, Eliya ayamba kudza ndithu, nadzakonza zinthu zonse; ndipo kwalembedwa bwanji za Mwana wa Munthu, kuti ayenera kumva zowawa zambiri ndi kuyesedwa chabe?


Kodi sanayenere Khristu kumva zowawa izi, ndi kulowa ulemerero wake?


Alowe mau amenewa m'makutu anu; pakuti Mwana wa Munthu adzaperekedwa m'manja a anthu.


Palibe wina andichotsera uwu, koma ndiutaya Ine ndekha. Ndili nayo mphamvu yakuutaya, ndi mphamvu ndili nayo yakuutenganso; lamulo ili ndinalandira kwa Atate wanga.


Yesu anayankha nati kwa iwo, Pasulani Kachisi uyu, ndipo masiku atatu ndidzamuutsa.


Ndipo monga Mose anakweza njoka m'chipululu, chotero Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa;


ngati tipirira, tidzachitanso ufumu ndi Iye: ngati timkana Iye, Iyeyunso adzatikana ife:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa