Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 9:29 - Buku Lopatulika

29 Ndipo Iye anati kwa iwo, Mtundu uwu sungathe kutuluka ndi kanthu kena konse, koma ndi kupemphera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Ndipo Iye anati kwa iwo, Mtundu uwu sukhoza kutuluka ndi kanthu kena konse, koma ndi kupemphera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Yesu adayankha kuti, “Mzimu wa mtundu umenewu, pokhapokha mutayamba mwapemphera mpamene mungautulutse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Iye anayankha kuti, “Mtundu uwu umatuluka pokhapokha mwapemphera ndi kusala kudya.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 9:29
17 Mawu Ofanana  

Ndipo ndinaika nkhope yanga kwa Ambuye Mulungu, kumfunsa Iye m'pemphero, ndi mapembedzero, ndi kusala, ndi ziguduli, ndi mapulusa.


Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu ina inzake isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo matsirizidwe ake a munthu uyo akhala oipa oposa mayambidwe ake. Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono.


Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani.


Ndipo pamene Iye adalowa m'nyumba, ophunzira ake anamfunsa m'tseri, kuti, Nanga bwanji sitinathe ife kuutulutsa?


Ndipo anachoka iwo kumeneko, napyola pakati pa Galileya; ndipo Iye sanafune kuti munthu adziwe.


Pomwepo upita nutenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoipa yoposa ndi uwu mwini; ndipo ilowa nikhalira komweko; ndipo makhalidwe otsiriza a munthu uyu aipa koposa oyambawo.


Ndipo pamene anawaikira akulu mosankha mu Mpingo uliwonse, ndi kupemphera pamodzi ndi kusala kudya, naikiza iwo kwa Ambuye amene anamkhulupirirayo.


koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.


m'chivutitso ndi m'cholemetsa, m'madikiro kawirikawiri, m'njala ndi ludzu, m'masalo a chakudya kawirikawiri, m'chisanu ndi umaliseche.


Za ichi ndinapemphera Ambuye katatu kuti chichoke kwa ine.


m'mikwingwirima, m'ndende, m'maphokoso, m'mavutitso, m'madikiro, m'masalo a chakudya;


mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,


ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa