Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 8:33 - Buku Lopatulika

33 Koma Iye anapotoloka, napenya ophunzira ake, namdzudzula Petro, nanena, Choka, pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; popeza susamalira zinthu za Mulungu, koma za anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Koma Iye anapotoloka, napenya ophunzira ake, namdzudzula Petro, nanena, Choka, pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; popeza susamalira zinthu za Mulungu, koma za anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Koma Yesu adacheuka, nayang'ana ophunzira ake ena aja, ndipo adadzudzula Petro. Adati, “Choka apa, iwe Satana! Maganizo akoŵa si maganizo a Mulungu ai, ndi maganizo a anthu chabe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Koma Yesu atatembenuka ndi kuyangʼana ophunzira ake, anamudzudzula Petro nati, “Choka pamaso panga Satana! Suganizira zinthu za Mulungu koma za anthu.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 8:33
24 Mawu Ofanana  

Koma Davide anati, Ndili ndi chiyani inu, ana a Zeruya inu, kuti muzikhala akutsutsana ndi ine lero? Kodi munthu adzaphedwa mu Israele lero? Sindidziwa kodi kuti ndine mfumu ya Israele lero?


Koma ananena naye, Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! Tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? Pa ichi chonse Yobu sanachimwe ndi milomo yake.


Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo: akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane: Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.


Usamamuda mbale wako mumtima mwako; umdzudzule munthu mnzako ndithu, usadzitengera uchimo chifukwa cha iye.


Koma Iye sanamyankhe mau amodzi. Ndipo ophunzira ake anadza, nampempha, nati, Mumuuze amuke; pakuti afuula pambuyo pathu.


Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.


Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.


Ndipo anawaunguzaunguza iwo akumzingawo, nanena, Taonani, amai wanga ndi abale anga.


Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.


Ndipo Ambuye anapotoloka, nayang'ana Petro. Ndipo Petro anakumbukira mau a Ambuye, kuti anati kwa iye, Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.


Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti, Ambuye Mulungu wako uzimgwadira, ndipo Iye yekhayekha uzimtumikira.


Koma Iye anapotoloka nawadzudzula.


kumpereka iye wochita chotere kwa Satana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m'tsiku la Ambuye Yesu.


chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko.


Iwo akuchimwa uwadzudzule pamaso pa onse, kuti otsalawo achite mantha.


Umboni uwu uli woona. Mwa ichi uwadzudzule mokalipa, kuti akakhale olama m'chikhulupiriro,


Popeza Khristu adamva zowawa m'thupi, mudzikonzere mtima womwewo; pakuti iye amene adamva zowawa m'thupi walekana nalo tchimo;


Musakonde dziko lapansi, kapena za m'dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye.


Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa