Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 7:31 - Buku Lopatulika

31 Ndipo anatulukanso m'maiko a ku Tiro, nadzera pakati pa Sidoni, kufikira ku nyanja ya Galileya, ndi kupyola pakati pa maiko a ku Dekapoli.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Ndipo anatulukanso m'maiko a ku Tiro, nadzera pakati pa Sidoni, kufikira ku nyanja ya Galileya, ndi kupyola pakati pa maiko a ku Dekapoli.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Yesu adachokanso ku dera lija la ku Tiro, namayenda kudutsa dera la ku Sidoni, kupita ku nyanja ya ku Galileya, kudzera pakati pa dera la Mizinda Khumi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Ndipo Yesu anachoka ku dera la Turo nadutsa pakati pa Sidoni, kutsikira ku nyanja ya Galileya kupita ku dera la Dekapoli.

Onani mutuwo Koperani




Marko 7:31
7 Mawu Ofanana  

Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsaida! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa inu zikadachitidwa mu Tiro ndi mu Sidoni, akadatembenuka mtima kalekale m'ziguduli ndi m'phulusa.


Ndipo pamene Yesu analikuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andrea, mbale wake, analikuponya khoka m'nyanja; popeza anali asodzi a nsomba.


Ndipo inamtsata mipingomipingo ya anthu ochokera ku Galileya, ndi ku Dekapoli ndi ku Yerusalemu, ndi ku Yudeya, ndi ku tsidya lija la Yordani.


Ndipo anamuka nayamba kulalikira ku Dekapoli zinthu zazikulu Yesu adamchitira iye; ndipo anthu onse anazizwa.


Ndipo Iye anauka nachoka kumeneko, nanka ku maiko a ku Tiro ndi Sidoni. Ndipo analowa m'nyumba, nafuna kuti asadziwe anthu; ndipo sanakhoze kubisika.


Ndipo anachoka kunka kunyumba kwake, napeza mwana atamgoneka pakama, ndi chiwanda chitatuluka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa