Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 7:28 - Buku Lopatulika

28 Koma iye anavomera nanena ndi Iye, Inde Ambuye; tingakhale tiagalu ta pansi pa gome tikudyako nyenyeswa za ana.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Koma iye anavomera nanena ndi Iye, Ine Ambuye; tingakhale tiagalu ta pansi pa gome tikudyako nyenyeswa za ana.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Apo maiyo adati, “Nzoonadi, Ambuye, koma suja ngakhale agalu omwe amakhala m'munsi mwa tebulo nkumadyako nyenyeswa zimene ataya ana?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Mayiyo anayankha kuti, “Inde Ambuye, koma ngakhale agalu amadya zomwe zimagwa pansi kuchokera pa tebulo la ana.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 7:28
15 Mawu Ofanana  

Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chao.


Yang'anani kwa Ine, mupulumutsidwe, inu malekezero onse a dziko; pakuti Ine ndine Mulungu, palibe wina.


inde, ati, Chili chinthu chopepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israele; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka ku malekezero a dziko lapansi.


Koma iye anati, Eetu, Ambuye, pakutinso tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye ao.


kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; chifukwa Iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.


Ndipo ananena naye, Baleka, ayambe akhuta ana; pakuti si kwabwino kuti titenge mkate wa ana, ndi kuutayira tiagalu.


Ndipo anati kwa iye, Chifukwa cha mau amene, muka; chiwanda chatuluka m'mwana wako wamkazi.


Pakuti kulibe kusiyana Myuda ndi Mgriki; pakuti Yemweyo ali Ambuye wa onse, nawachitira zolemera onse amene aitana pa Iye;


Kapena Mulungu ndiye wa Ayuda okhaokha kodi? Si wao wa amitundunso kodi? Eya, wa amitundunso:


Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa