Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 7:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo ananena naye, Baleka, ayambe akhuta ana; pakuti si kwabwino kuti titenge mkate wa ana, ndi kuutayira tiagalu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo ananena naye, Baleka, athange akhuta ana; pakuti si kwabwino kuti titenge mkate wa ana, ndi kuutayira tiagalu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Koma Yesu adamuyankha kuti, “Ai, alekeni ana ayambe adya nkukhuta. Sibwino kutenga chakudya cha ana nkuponyera agalu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Iye anamuwuza kuti, “Choyamba asiye ana adye zimene akuzifuna, pakuti si kwabwino kutenga buledi wa ana ndi kuponyera agalu awo.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 7:27
8 Mawu Ofanana  

Awa amene, khumi ndi awiriwa, Yesu anawatumiza, nawalangiza ndi kuti, Musapite kunjira ya kwa anthu akunja, ndi m'mudzi wa Asamariya musamalowamo:


Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.


Koma mkaziyo anali Mgriki, mtundu wake Msiro-Fenisiya. Ndipo anampempha Iye kuti atulutse chiwanda m'mwana wake.


Koma iye anavomera nanena ndi Iye, Inde Ambuye; tingakhale tiagalu ta pansi pa gome tikudyako nyenyeswa za ana.


Ndipo anati kwa ine, Pita; chifukwa Ine ndidzakutuma iwe kunka kutali kwa amitundu.


Ndipo ndinena kuti Khristu anakhala mtumiki wa mdulidwe, chifukwa cha choonadi cha Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo opatsidwa kwa makolo,


kuti nthawi ija munali opanda Khristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israele, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m'dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa