Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 6:48 - Buku Lopatulika

48 Ndipo pakuwaona ali kuvutidwa ndi kupalasa, pakuti mphepo inadza nikomana nao, pa ulonda wachinai wa usiku Iye anadza kwa iwo, alikuyenda pamwamba pa nyanja; nati awapitirire;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

48 Ndipo pakuwaona ali kuvutidwa ndi kupalasa, pakuti mphepo inadza nikomana nao, pa ulonda wachinai wa usiku Iye anadza kwa iwo, alikuyenda pamwamba pa nyanja; nati awapitirire;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

48 Ndiye adaona ophunzira aja akuvutika ndi kupalasa chombo, chifukwa anali atayang'anana ndi mphepo. M'mamaŵa kukali mbuu, Yesu adadza kwa iwo, Iye akuyenda pa madzi panyanjapo, nkumafuna kuŵapitirira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

48 Iye anaona ophunzira ake akuvutika popalasa bwato, chifukwa mphepo imawomba mokumana nawo. Pa nthawi ya mʼbandakucha Iye anafika kwa iwo akuyenda pa nyanja. Anali pafupi kuwapitirira,

Onani mutuwo Koperani




Marko 6:48
16 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Taonanitu, Ambuye anga, tembenukanitu, kulowa m'nyumba mwa kapolo wanu, mugone usiku wonse, mutsuke mapazi anu, ndipo mudzalawira m'mawa kunka ulendo wanu. Ndipo anati, Iai; koma tigone m'khwalalamu usiku wonse.


Ndipo iye anati Ndileke ndimuke, chifukwa kulinkucha. Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine.


Woyala thambo yekha, naponda pa mafunde a panyanja.


Amene alumikiza mitanda ya zipinda zake m'madzi; naika makongwa akhale agaleta ake; nayenda pa mapiko a mphepo.


Yehova Wam'mwamba ndiye wamphamvu, wakuposa mkokomo wa madzi ambiri, ndi mafunde olimba a nyanja.


Ndipo kunali, ulonda wa mamawa, Yehova ali m'moto ndi m'mtambo njo anapenyera pa ulendo wa Aejipito, nauvuta ulendo wa Aejipito.


Iwe wosautsidwa, wobelukabeluka ndi namondwe, wosatonthola mtima, taona, ndidzakhazika miyala yako m'mawangamawanga abwino, ndi kukhazika maziko ako ndi masafiro.


Koma pomwepo ngalawa idafika pakati pa nyanja, yozunzika ndi mafunde; pakuti mphepo inadza mokomana nao.


Koma dziwani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yiti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibooledwe.


Chifukwa chake dikirani; pakuti simudziwa inu nthawi yake yakubwera mwini nyumba, kapena madzulo, kapena pakati pausiku, kapena pakulira tambala, kapena mamawa;


Ndipo pofika madzulo ngalawa inali pakati pa nyanja, ndi Iye yekha pamtunda.


koma iwo, pamene anamuona alikuyenda panyanja, anayesa kuti ndi mzukwa, nafuula:


Ndipo akadza ulonda wachiwiri, kapena wachitatu, nakawapeza atero, odala amenewa.


Ndipo anayandikira kumudzi umene analikupitako; ndipo anachita ngati anafuna kupitirira.


amene sanabadwe ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.


Ndipo m'mawa mwake Saulo anagawa anthu magulu atatu; ndipo iwowa anafika pakati pa zithandozo mu ulonda wa mamawa, nakantha Aamoni kufikira kutentha kwa dzuwa. Ndipo otsalawo anabalalika, osatsala pamodzi ngakhale awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa