Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 6:30 - Buku Lopatulika

30 Ndipo atumwi anasonkhana kwa Yesu; namuuza zilizonse adazichita, ndi zonse adaziphunzitsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Ndipo atumwi anasonkhana kwa Yesu; namuuza zilizonse adazichita, ndi zonse adaziphunzitsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Atumwi aja adabwerera kwa Yesu namufotokozera zonse zimene adaachita ndi kuphunzitsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Atumwi anasonkhana mozungulira Yesu namufotokozera zonse zomwe anachita ndi kuphunzitsa.

Onani mutuwo Koperani




Marko 6:30
17 Mawu Ofanana  

Mnyamatayo ndipo anamuuza Isaki zonse anazichita.


Ndipo maina ao a atumwiwo khumi ndi awiri ndi awa: woyamba Simoni wotchedwa Petro, ndi Andrea mbale wake; Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake;


Ndipo anaika khumi ndi awiri, kuti akhale ndi Iye, ndi kuti akawatume kulalikira,


Ndipo m'mene ophunzira ake anamva, anadza nanyamula mtembo wake nauika m'manda.


Ndipo makumi asanu ndi awiri aja anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m'dzina lanu.


Ndipo atumwi anati kwa Ambuye, Mutionjezere chikhulupiriro.


Ndipo itadza nthawi yake, Iye anakhala pachakudya, ndi ophunzira pamodzi ndi Iye.


Koma panali Maria wa Magadala, ndi Yohana, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi akazi ena pamodzi nao amene ananena izi kwa atumwiwo.


Ndipo kutacha, anaitana ophunzira ake; nasankha mwa iwo khumi ndi awiri, amene anawatchanso dzina lao atumwi:


Ndipo atabwera atumwi, anamfotokozera Iye zonse anazichita. Ndipo Iye anawatenga, napatuka nao pa okha kunka kumzinda dzina lake Betsaida.


Ndipo anayesa maere pa iwo; ndipo anagwera Matiasi; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa