Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 6:22 - Buku Lopatulika

22 ndipo pamene mwana wamkazi wa Herodiasi analowa yekha navina, anakondwetsa Herode ndi iwo akukhala naye pachakudya; ndipo mfumuyo inati kwa buthulo, Tapempha kwa ine chilichonse uchifuna, ndidzakupatsa iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 ndipo pamene mwana wamkazi wa Herodiasi analowa yekha navina, anakondwetsa Herode ndi iwo akukhala naye pachakudya; ndipo mfumuyo inati kwa buthulo, Tapempha kwa ine chilichonse uchifuna, ndidzakupatsa iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Tsono mwana wamkazi wa Herodiasi adaloŵa, nayamba kuvina. Kuvinako adakondweretsa nako kwambiri Herode ndi amene adaali naye paphwandopo. Pamenepo mfumuyo idauza mtsikanayo kuti, “Undipemphe chilichonse chimene ukufuna, ine ndikupatsa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Mwana wamkazi wa Herodia atabwera ndi kudzavina, anakondweretsa Herode ndi alendo ake a pa mphwandopo. Mfumu inati kwa mtsikanayo, “Undipemphe chilichonse chimene ukuchifuna, ndipo ndidzakupatsa.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 6:22
6 Mawu Ofanana  

Belisazara, pakulawa vinyo, anati abwere nazo zotengera za golide ndi siliva adazichotsa Nebukadinezara atate wake ku Kachisi ali ku Yerusalemu, kuti mfumu ndi akulu ake, akazi ake ndi akazi ake aang'ono, amweremo.


Ndi kuti, Tinakulizirani inu zitoliro, ndipo inu simunavine; tinabuma maliro, ndipo inu simunalire.


Pakuti Herode adamgwira Yohane, nammanga, namuika m'nyumba yandende chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake Filipo.


Koma pakufika tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiasi anavina pakati pao, namkondweretsa Herode.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa