Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 6:17 - Buku Lopatulika

17 Pakuti Herode, mwini yekha, adatuma anthu namgwira Yohane, nammanga m'nyumba yandende, chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo mbale wake; chifukwa adamkwatira iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Pakuti Herode, mwini yekha, adatuma anthu namgwira Yohane, nammanga m'nyumba yandende, chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo mbale wake; chifukwa adamkwatira iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Pajatu Herode kale adaatuma asilikali ake kuti akagwire Yohane, akammange ndi kumponya m'ndende. Adaachita zimenezi chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo, mbale wake. Ndiye kuti Herode anali atamkwatira maiyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Pakuti Herode iye mwini analamula kuti amumange Yohane ndi kumuyika mʼndende. Anachita izi chifukwa cha Herodia, mkazi wa mʼbale wake Filipo, amene iye anamukwatira.

Onani mutuwo Koperani




Marko 6:17
7 Mawu Ofanana  

Koma Yohane, pakumva m'nyumba yandende ntchito za Khristu, anatumiza ophunzira ake mau,


Ndipo pamene Yesu anamva kuti anampereka Yohane, anamuka kulowa ku Galileya;


Koma Herode pamene anamva, ananena, Yohane amene ndamdula mutu, wauka iyeyo.


Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio Kaisara, pokhala Pontio Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lisaniasi chiwanga cha Abilene;


Pakuti Yohane sanaikidwe m'ndende.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa