Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 5:40 - Buku Lopatulika

40 Ndipo anamseka Iye pwepwete. Koma Iye anawatulutsa onse, natenga atate wa mwana, ndi amake, ndi ajawo anali naye, nalowa m'mene munali mwanayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

40 Ndipo anamseka Iye pwepwete. Koma Iye anawatulutsa onse, natenga atate wa mwana, ndi amake, ndi ajawo anali naye, nalowa m'mene munali mwanayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

40 Pamenepo anthuwo adayamba kumseka monyodola. Iye adaŵatulutsira panja onse, nangotenga bambo wake ndi mai wake wa mwanayo, ndiponso amene adaali naye aja, nkuloŵa kuchipinda kumene kunali mwana uja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

40 Koma anamuseka Iye. Atawatulutsa onse panja, Iye anatenga abambo ndi amayi ake a mwanayo ndi ophunzira omwe anali naye, ndipo analowa mʼmene munali mwanayo.

Onani mutuwo Koperani




Marko 5:40
14 Mawu Ofanana  

Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene amayenera kukwatira ana ake aakazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mzindawu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka.


Nalowa Elisa, nadzitsekera awiriwa, napemphera kwa Yehova.


Koma Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapolo Mwamoniyo, ndi Gesemu Mwarabu, anamva natiseka pwepwete, natipeputsa, nati, Chiyani ichi muchichita? Mulikupandukira mfumu kodi?


Ndine ngati munthu wosekedwa ndi mnansi wake, ndinaitana kwa Mulungu, ndipo anandiyankha; munthu wolungama wangwiro asekedwa.


Onse akundipenya andiseka; akwenzula, apukusa mutu, nati,


si chimene chilowa m'kamwa mwake chiipitsa munthu; koma chimene chituluka m'kamwa mwake, ndicho chiipitsa munthu.


Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.


Ndipo m'mene atalowa, ananena nao, Mubuma ndi kulira bwanji? Mwana sanafe, koma ali m'tulo.


Ndipo anagwira dzanja lake la mwana, nanena kwa iye, Talita koumi, ndiko kunena posandulika, Buthu, ndinena ndi iwe, Uka.


Koma Afarisi, ndiwo okonda ndalama, anamva izi zonse; ndipo anamseka.


Ndipo pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za chimenechi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa