Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 5:39 - Buku Lopatulika

39 Ndipo m'mene atalowa, ananena nao, Mubuma ndi kulira bwanji? Mwana sanafe, koma ali m'tulo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Ndipo m'mene atalowa, ananena nao, Mubuma ndi kulira bwanji? Mwana sanafe, koma ali m'tulo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Iye ataloŵa, adaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita phokoso lonseli ndi kubuma? Mwanayutu sadamwalire ai, ali m'tulo chabe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Analowa nati kwa iwo, “Mukuchita phokoso ndi kulira chifukwa chiyani? Mwanayu sanamwalire koma ali mtulo.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 5:39
9 Mawu Ofanana  

Ndipo ambiri a iwo ogona m'fumbi lapansi adzauka, ena kunka kumoyo wosatha, ndi ena kumanyazi ndi mnyozo wosatha.


ananena, Tulukani, pakuti kabuthuko sikanafe koma kali m'tulo. Ndipo anamseka Iye pwepwete.


Ndipo anafika kunyumba kwake kwa mkulu wa sunagoge; ndipo anaona chipiringu, ndi ochita maliro, ndi akukuwa ambiri.


Ndipo anamseka Iye pwepwete. Koma Iye anawatulutsa onse, natenga atate wa mwana, ndi amake, ndi ajawo anali naye, nalowa m'mene munali mwanayo.


Ndipo potsikirako Paulo, anamgwera namfungatira, nati, Musachite phokoso, pakuti moyo wake ulipo.


Chifukwa chake ambiri mwa inu afooka, nadwala, ndipo ambiri agona.


amene anafa m'malo mwathu, kuti, tingakhale tidikira, tingakhale tigona, tikakhale ndi moyo pamodzi ndi Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa