Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 5:35 - Buku Lopatulika

35 M'mene iye ali chilankhulire, anafika a kunyumba ya mkulu wa sunagoge, nanena, kuti, Mwana wako wafa; uvutiranjinso Mphunzitsi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 M'mene iye ali chilankhulire, anafika a kunyumba ya mkulu wa sunagoge, nanena, kuti, Mwana wako wafa; uvutiranjinso Mphunzitsi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Yesu akulankhulabe, kudafika anthu kuchokera kunyumba kwa mkulu uja. Adamuuza mkuluyo kuti, “Mwana uja watsirizika. Musaŵavutenso Aphunzitsiŵa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Pamene Yesu ankayankhulabe, amuna ena anafika kuchokera ku nyumba ya Yairo, mkulu wa sunagoge. Iwo anati, “Mwana wanu wamkazi wamwalira, muvutitsiranjinso aphunzitsiwa?”

Onani mutuwo Koperani




Marko 5:35
13 Mawu Ofanana  

Koma Yesu podziwa, anati kwa iwo, Mumvutiranji mkaziyu? Popeza andichitira Ine ntchito yabwino.


Nati Iye, Mukani kumzinda kwa munthu wina wake, mukati kwa Iye, Mphunzitsi anena, Nthawi yanga yayandikira; ndidzadya Paska kwanu pamodzi ndi ophunzira anga.


M'mene Iye analikulankhula nao zinthu zimenezo, onani, anadza munthu mkulu, namgwadira Iye, nanena, Wamwalira tsopanoli mwana wanga wamkazi, komatu mudze muike dzanja lanu pa iye, ndipo adzakhala ndi moyo.


Ndipo pamene Iye anatuluka kutsata njira, anamthamangira munthu, namgwadira Iye, namfunsa, Mphunzitsi wabwino, ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?


Ndipo anadzako mmodzi wa akulu a sunagoge, dzina lake Yairo; ndipo pakuona Iye, anagwada pa mapazi ake, nampempha kwambiri,


M'mene Iye anali chilankhulire, anadza wina wochokera kwa mkulu wa sunagoge, nanena, Mwana wako wafa; usamvute Mphunzitsi.


Ndipo Marita anati kwa Yesu, Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa.


Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo;


Ndipo m'mene anati ichi anachoka naitana Maria mbale wake m'tseri, ndi kuti, Wafika Mphunzitsi, akuitana iwe.


Pomwepo Maria, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona Iye, anagwa pa mapazi ake, nanena ndi Iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira.


Yesu ananena, Chotsani mwala. Marita, mlongo wake wa womwalirayo, ananena ndi Iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anai.


Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo ilipo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa