Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 5:27 - Buku Lopatulika

27 m'mene iye anamva mbiri yake ya Yesu, anadza m'khamu kumbuyo kwake, nakhudza chovala chake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 m'mene iye anamva mbiri yake ya Yesu, anadza m'khamu kumbuyo kwake, nakhudza chovala chake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Maiyo anali atamva za Yesu. Tsono adaloŵa m'chinamtindi cha anthu chija, nkuphaphatiza mpaka kukafika cha kumbuyo kwa Yesu, nakhudza chovala chake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Atamva za Yesu, anabwera kumbuyo kwake mʼgulu la anthu ndipo anakhudza mkanjo wake,

Onani mutuwo Koperani




Marko 5:27
7 Mawu Ofanana  

Ndipo anthu, pakuika maliro a munthu wina, anaona gulu la nkhondo, naponya mtembo m'manda mwa Elisa; koma pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, wakufayo anauka, naima chilili.


ndipo anampempha Iye, kuti akhudze mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.


ndipo anamva zowawa zambiri ndi asing'anga ambiri, nalipira zonse anali nazo osachira pang'ono ponse, koma makamaka nthenda yake idakula,


Pakuti ananena iye, Ngati ndikakhudza ngakhale zovala zake ndidzapulumutsidwa.


Ndipo kumene konse adalowa Iye m'midzi, kapena m'mizinda, kapena kumadera, anthu anagoneka odwala pamisika, nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.


kotero kuti anamuka nazo kwa odwala nsalu zopukutira ndi za pantchito, zochokera pathupi pake, ndipo nthenda zinawachokera, ndi ziwanda zinatuluka.


kotero kuti ananyamulanso natuluka nao odwala kumakwalala, nawaika pamakama ndi pamphasa, kuti, popita Petro, ngakhale chithunzi chake chigwere wina wa iwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa