Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 4:38 - Buku Lopatulika

38 Ndipo Iye mwini anali kutsigiro, nagona tulo pamtsamiro; ndipo anamuutsa Iye nanena kwa Iye, Mphunzitsi, kodi simusamala kuti titayika ife?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

38 Ndipo Iye mwini anali kutsigiro, nagona tulo pamtsamiro; ndipo anamuutsa Iye nanena kwa Iye, Mphunzitsi, kodi simusamala kuti titayika ife?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

38 Koma nthaŵi imeneyo Yesu anali kumbuyo m'chombomo, ali m'tulo atatsamira mtsamiro. Pamenepo ophunzira aja adamudzutsa, adati, “Aphunzitsi, kodi simukusamalako kuti tikumira?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

38 Pa nthawi imeneyi Yesu anali akugona atatsamira pilo kumbuyo kwa bwato. Ophunzira anamudzutsa nati kwa Iye, “Aphunzitsi, kodi simukusamala kuti timira?”

Onani mutuwo Koperani




Marko 4:38
22 Mawu Ofanana  

Tayang'anani kunsi kuchokera kumwamba, taonani pokhala panu poyera, ndi pa ulemerero wanu, changu chanu ndi ntchito zanu zamphamvu zili kuti? Mwanditsekerezera zofunafuna za mtima wanu ndi chisoni chanu.


Kodi mudzadziletsa pa zinthuzi, Yehova? Kodi Inu mudzakhala chete ndi kutivutitsa ife zolimba?


Inde, pofuula ine ndi kuitana andithandize amakaniza pemphero langa.


Ndipo anatumiza kwa Iye ophunzira ao, pamodzi ndi Aherode, amene ananena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu moona ndithu, ndipo simusamala munthu aliyense; pakuti simuyang'anira pa nkhope ya anthu.


Ndipo iwo anadza, namuutsa Iye, nanena, Ambuye, tipulumutseni, tilikutayika.


Ndipo panauka namondwe wamkulu wa mphepo, ndi mafunde anagavira mungalawa, motero kuti ngalawa inayamba kudzala.


Ndipo anauka, nadzudzula mphepo, nati kwa nyanja, kuti, Tonthola, khala bata. Ndipo mphepo inaleka, ndipo kunagwa bata lalikulu.


Ndipo anadza kwa Iye, namuutsa, nanena, Ambuye, Ambuye, titayika. Ndipo anauka, nadzudzula mphepo ndi mafunde ake a madzi; pomwepo zinaleka, ndipo panagwa bata.


ndipo pamenepo panali chitsime cha Yakobo. Ndipo Yesu, popeza analema ndi ulendo wake, motero anakhala pachitsime.


Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m'zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu.


Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.


ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa