Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 4:37 - Buku Lopatulika

37 Ndipo panauka namondwe wamkulu wa mphepo, ndi mafunde anagavira mungalawa, motero kuti ngalawa inayamba kudzala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 Ndipo panauka namondwe wamkulu wa mphepo, ndi mafunde anagavira mungalawa, motero kuti ngalawa inayamba kudzala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 Tsono padauka namondwe woopsa. Mafunde ankaloŵa m'chombomo, kotero kuti chidaayamba kudzaza ndi madzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 Mphepo yamkuntho inabuka, ndipo mafunde anawomba bwatolo, kotero kuti linali pafupi kumira.

Onani mutuwo Koperani




Marko 4:37
11 Mawu Ofanana  

Nati Yehova kwa Satana, Taona, zonse ali nazo zikhale m'dzanja mwako; pa iye pokha usatambasula dzanja lako. Natuluka Satana pamaso pa Yehova.


ndipo taonani, inadza mphepo yaikulu yochokera kuchipululu, niomba pangodya zonse zinai za nyumbayo, nigwa pa anyamatawo, nafa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.


Koma Yehova anautsa chimphepo chachikulu panyanja, ndipo panali namondwe wamkulu panyanja, ndi chombo chikadasweka.


Ndipo posiya khamulo anamtenga apite nao, monga momwe anali, mungalawa. Ndipo panali ngalawa zina pamodzi ndi Iye.


Ndipo Iye mwini anali kutsigiro, nagona tulo pamtsamiro; ndipo anamuutsa Iye nanena kwa Iye, Mphunzitsi, kodi simusamala kuti titayika ife?


Koma pofika pamalo pokomana mafunde awiri, anatsamitsapo ngalawa; ndipo kulikulu kunatsama, ndi kukhala kosasunthika, koma kumakaliro kunasweka ndi mphamvu ya mafunde.


Katatu ndinamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndinaponyedwa miyala, katatu ndinatayika posweka chombo, ndinakhala m'kuya tsiku limodzi usana ndi usiku;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa