Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 16:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo iwowa anatuluka, nalalikira ponseponse, ndipo Ambuye anachita nao pamodzi, natsimikiza mau ndi zizindikiro zakutsatapo. Amen.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo iwowa anatuluka, nalalikira ponseponse, ndipo Ambuye anachita nao pamodzi, natsimikiza mau ndi zizindikiro zakutsatapo. Amen.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Tsono ophunzira aja adanka nalalika ponseponse. Ambuye ankagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo ankatsimikiza mau ao ndi zozizwitsa zimene ankachita.]

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Pamenepo ophunzira aja anapita ndi kukalalikira ponseponse, ndipo Ambuye anagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo anatsimikizira mawuwo ndi zizindikiro zimene ankachita.

Onani mutuwo Koperani




Marko 16:20
15 Mawu Ofanana  

Pamenepo Ambuye Yesu, atatha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala padzanja lamanja la Mulungu.


Popeza ambiri anayesa kulongosola nkhani ya zinthu zinachitika pakati pa ife,


monga anazipereka kwa ife iwo amene anakhala mboni ndi atumiki a mau,


Chifukwa chake anakhala nthawi yaikulu nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye, amene anachitira umboni mau a chisomo chake, napatsa zizindikiro ndi zozizwa kuti zichitidwe ndi manja ao.


m'mene mutambasula dzanja lanu kukachiritsa; ndi kuti zizindikiro ndi zozizwa zichitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu.


Ndipo mwa manja a atumwi zizindikiro ndi zozizwa zambiri zinachitidwa pa anthu; ndipo anali onse ndi mtima umodzi m'khonde la Solomoni.


mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu;


Ndipo ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu,


tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife;


pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa