Marko 15:36 - Buku Lopatulika36 Ndipo anathamanga wina, nadzaza chinkhupule ndi vinyo wosasa, nachiika pabango, namwetsa Iye, nanena, Lekani; tione ngati Eliya adza kudzamtsitsa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201436 Ndipo anathamanga wina, nadzaza chinkhupule ndi vinyo wosasa, nachiika pabango, namwetsa Iye, nanena, Lekani; tione ngati Eliya adza kudzamtsitsa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa36 Motero wina adathamanga nakaviika chinkhupule m'vinyo wosasa, nkuchitsomeka ku bango nampatsira, kuti amwe. Anzakewo adati, “Taima, tiwone ngati Eliyayo abweredi kudzamtsitsa.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero36 Munthu wina anathamanga, natenga chinkhupule atachiviyika mu vinyo wosasa, anachizika ku mtengo, ndi kumupatsa Yesu kuti amwe. Munthuyo anati, “Musiyeni yekha tsopano. Tiyeni tione ngati Eliya angabwere kudzamutsitsa.” Onani mutuwo |