Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 15:32 - Buku Lopatulika

32 Atsike tsopano pamtanda, Khristu mfumu ya Israele, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupachikidwa naye anamlalatira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Atsike tsopano pamtanda, Khristu mfumu ya Israele, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupachikidwa naye anamlalatira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Uja ankati ndi Mpulumutsi wolonjezedwayu, Mfumu ya Aisraele, atatsikatu tsopano pamtandapa, kuti tiwone ndi kumkhulupirira!” Ndiponso amene adaŵapachika pamodzi naye aja ankamunyoza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Musiyeni Khristu, Mfumu ya Aisraeli, atsike tsopano kuchoka pa mtanda, kuti ife tione ndi kukhulupirira.” Iwonso amene anapachikidwa naye pamodzi anamulalatira.

Onani mutuwo Koperani




Marko 15:32
16 Mawu Ofanana  

Atero Yehova, mfumu ya Israele ndi Mombolo wake, Yehova wa makamu, Ine ndili woyamba ndi womaliza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu.


Yehova wachotsa maweruzo ako, anataya kunja mdani wako; mfumu ya Israele, Yehova, ali pakati pako, sudzaopanso choipa.


Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.


Motero mibadwo yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide ndiyo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa kutengedwa kunka ku Babiloni mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa kutengedwa kunka ku Babiloni kufikira kwa Khristu mibadwo khumi ndi inai.


Anapulumutsa ena, sangathe kudzipulumutsa yekha. Ndiye mfumu ya Aisraele; atsike tsopano pamtandapo, ndipo tidzamkhulupirira Iye.


Ndiponso achifwambawo opachikidwa pamodzi ndi Iye, anamlalatira Iye mau amodzimodzi.


Ndipo lembo la mlandu wake linalembedwa pamwamba, MFUMU YA AYUDA.


Ndipo anapachika pamodzi ndi Iye achifwamba awiri; mmodzi kudzanja lake lamanja ndi wina kulamanzere.


Natanaele anayankha Iye, Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu mfumu ya Israele.


anatenga makwata a kanjedza, natuluka kukakomana ndi Iye, nafuula, Hosana; wolemekezeka Iye wakudza m'dzina la Ambuye, ndiye mfumu ya Israele.


Nanga bwanji ngati ena sanakhulupirire? Kodi kusakhulupirira kwao kuyesa chabe chikhulupiriko cha Mulungu?


ndiwo amene adasokera kunena za choonadi, ponena kuti kuuka kwa akufa kwachitika kale, napasula chikhulupiriro cha ena.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa