Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 15:26 - Buku Lopatulika

26 Ndipo lembo la mlandu wake linalembedwa pamwamba, MFUMU YA AYUDA.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndipo lembo la mlandu wake linalembedwa pamwamba, MFUMU YA AYUDA.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Mau osonyeza mlandu womuphera, adaaŵalemba motere, “Mfumu ya Ayuda.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Chikwangwani cholembedwapo mlandu wake chinali choti: mfumu ya ayuda.

Onani mutuwo Koperani




Marko 15:26
14 Mawu Ofanana  

Koma Ine ndadzoza mfumu yanga Pa Ziyoni, phiri langa loyera.


Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani; chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.


Mtima wa mfumu uli m'dzanja la Yehova ngati mitsinje ya madzi; aulozetsa komwe afuna.


Koma iye safuna chotero, ndipo mtima wake suganizira chotero, koma mtima wake ulikufuna kusakaza, ndi kuduladula amitundu osawerengeka.


ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse;


Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.


nati, Ali kuti amene anabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.


Ndipo anaika pamwamba pamutu pake mlandu wake wolembedwa: UYU NDI YESU MFUMU YA AYUDA.


Ndipo Pilato anamfunsa Iye, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo anayankha, nanena naye, Mwatero.


Ndipo anapachika pamodzi ndi Iye achifwamba awiri; mmodzi kudzanja lake lamanja ndi wina kulamanzere.


Atsike tsopano pamtanda, Khristu mfumu ya Israele, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupachikidwa naye anamlalatira.


Ndipo Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu; koma Yehova Mulungu wanu anakusandulizirani tembererolo likhale mdalitso, popeza Yehova Mulungu wanu anakukondani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa