Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 15:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo Pilato pofuna kuwakhazika mtima anthuwo, anawamasulira Barabasi, napereka Yesu, atamkwapula, akampachike pamtanda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo Pilato pofuna kuwakhazika mtima anthuwo, anawamasulira Barabasi, napereka Yesu, atamkwapula, akampachike pamtanda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Choncho Pilato, pofuna kukondwetsa anthuwo, adaŵamasulira Barabasi, nalamula kuti Yesu akwapulidwe. Pambuyo pake adampereka kuti akampachike pa mtanda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Pilato pofuna kuwakondweretsa anthuwo, anawamasulira Baraba. Analamula kuti Yesu akwapulidwe mwankhanza, ndipo anamupereka kuti akapachikidwe.

Onani mutuwo Koperani




Marko 15:15
17 Mawu Ofanana  

Olima analima pamsana panga; anatalikitsa mipere yao.


Kwezekani m'mwambamwamba, Mulungu; ulemerero wanu ukhale pamwamba m'dziko lonse lapansi.


Kuopa anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.


Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisire nkhope yanga manyazi ndi kulavulidwa.


nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika; ndipo Iye adzaukitsidwa tsiku lachitatu.


Pomwepo iye anamasulira iwo Barabasi, koma anakwapula Yesu, nampereka Iye kuti akampachike pamtanda.


ndipo adzamnyoza Iye, nadzamthira malovu, nadzamkwapula Iye, nadzamupha; ndipo pofika masiku atatu adzauka.


Ndipo Pilato ananena nao, Pakuti Iye anachita choipa chotani? Koma iwo anafuulitsatu, Mpachikeni Iye.


ndipo atamkwapula adzamupha Iye; ndipo tsiku lachitatu adzauka.


Chifukwa chake ndidzamkwapula ndi kummasula Iye.


Pamenepo tsono Pilato anatenga Yesu, namkwapula.


Ndipo pamenepo anampereka Iye kwa iwo kuti ampachike. Pamenepo anatenga Yesu;


Koma zitapita zaka ziwiri Porkio Fesito analowa m'malo a Felikisi; ndipo Felikisi pofuna kukonda Ayuda anamsiya Paulo m'nsinga.


Koma Fesito pofuna kuyesedwa wachisomo ndi Ayuda, anayankha kwa Paulo, nati, Kodi ufuna kukwera kunka ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa ndi ine pomwepo kunena za zinthu izi?


Koma wina wa atumwi sindinamuone, koma Yakobo mbale wa Ambuye.


amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa