Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 14:70 - Buku Lopatulika

70 Koma anakananso. Ndipo patapita kamphindi, akuimirirapo ananenanso ndi Petro, Zedi uli wa awo; pakutinso uli Mgalileya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

70 Koma anakananso. Ndipo patapita kamphindi, akuimirirapo ananenanso ndi Petro, Zedi uli wa awo; pakutinso uli Mgalileya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

70 Koma Petro adakananso. Patangopita kanthaŵi, anthu amene adaali pamenepo adamuuza Petro kuti, “Ndithu nawenso ndiwe wa gulu lomweli. Kodi kwanu si ku Galileya iwe?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

70 Anakananso kachiwiri. Patapita kanthawi pangʼono, amene anayimirira pafupi anati kwa Petro, “Zoonadi ndiwe mmodzi wa iwo, pakuti ndiwe mu Galileya.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 14:70
8 Mawu Ofanana  

Koma anakana, nanena, Sindidziwa kapena kumvetsa chimene uchinena iwe; ndipo anatuluka kunka kuchipata; ndipo tambala analira.


Ndipo anamuona mdzakaziyo, nayambanso kunena ndi iwo akuimirirapo, Uyu ngwa awo.


Koma iye anayamba kutemberera, ndi kulumbira, Sindimdziwa munthuyu mulikunena.


Ndipo anadabwa onse, nazizwa, nanena, Taonani, awa onse alankhulawa sali Agalileya kodi?


pamenepo anati kwa iye, Unene tsono Shiboleti; ndipo akati, Siboleti, osakhoza kutchula bwino, amgwira namupha padooko pomwe pa Yordani; ndipo anagwa a Efuremu nthawi ija, zikwi makumi anai mphambu ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa