Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 14:44 - Buku Lopatulika

44 Ndipo wakumpereka Iye anawapatsa chizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsompsona, ndiyetu; mgwireni munke naye chisungire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

44 Ndipo wakumpereka Iye anawapatsa chizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsompsona, ndiyetu; mgwireni munke naye chisungire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

44 Wodzampereka uja anali ataŵauza chizindikiro kuti, “Yemwe ndikamumpsompsoneyo, ndi ameneyo. Mukamgwire nkupita naye, osamtaya.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

44 Tsopano womupereka anapangana chizindikiro ndi iwo kuti: “Amene ndikapsompsone ndi iyeyo; mukamugwire ndi kumutenga ali womangidwa.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 14:44
13 Mawu Ofanana  

Ndipo mwaziwo udzakhala chizindikiro kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko la Ejipito.


Kulasa kwa bwenzi kuli kokhulupirika; koma mdani apsompsona kawirikawiri.


Ukani, timuke; taonani, iye wakundipereka wayandikira.


Ndipo pomwepo, Iye ali chilankhulire, anadza Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndipo pamodzi naye khamu la anthu, ali nao malupanga ndi mikunkhu, ochokera kwa ansembe aakulu ndi alembi ndi akulu.


Ndipo atafika, pomwepo anadza kwa Iye, nanena, Rabi; nampsompsonetsa.


Pamene anawaonetsa mikwingwirima yambiri, anawaika m'ndende, nauza mdindo kuti awasunge bwino.


osaopa adani m'kanthu konse, chimene chili kwa iwowa chisonyezo cha chionongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu;


Ndipereka moni ndi dzanja langa Paulo; ndicho chizindikiro m'kalata aliyense; ndiko kulemba kwanga.


Ndipo tsopano, mundilumbiriretu kwa Yehova, popeza ndakuchitirani chifundo, kuti inunso mudzachitira chifundo a m'nyumba ya atate wanga ndi kundipatsa chizindikiro choona,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa