Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 14:14 - Buku Lopatulika

14 ndipo kumene akalowako iye, munene naye mwini nyumba, Mphunzitsi anena, Chilikuti chipinda cha alendo changa, m'menemo ndikadye Paska ndi ophunzira anga?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 ndipo kumene akalowako iye, munene naye mwini nyumba, Mphunzitsi anena, Chilikuti chipinda cha alendo changa, m'menemo ndikadye Paska ndi ophunzira anga?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Kunyumba kumene ati akaloŵe, mukauze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa kuti, kodi nchiti chipinda cha alendo choti Iwowo adzadyeremo phwando la Paska ndi ophunzira ao?’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Kawuzeni mwini nyumba imene iye akalowemo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa: kodi chili kuti chipinda changa cha alendo, kumene ndidyere Paska ndi ophunzira anga?’

Onani mutuwo Koperani




Marko 14:14
8 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene Iye anatuluka kutsata njira, anamthamangira munthu, namgwadira Iye, namfunsa, Mphunzitsi wabwino, ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?


Ndipo munthu akati kwa inu, Mutero bwanji? Katini, Ambuye amfuna iye; ndipo pomwepo adzamtumiza kuno.


Ndipo anatuma awiri a ophunzira ake, nanena nao, Lowani m'mzinda, ndipo adzakomana nanu munthu wakusenza mtsuko wa madzi; mumtsate iye;


Ndipo iye yekha adzakusonyezani chipinda chapamwamba chachikulu choyalamo ndi chokonzedwa; ndipo m'menemo mutikonzere.


Ndipo mukanene kwa mwini nyumbayo, Mphunzitsi anena nawe, Chipinda cha alendo chili kuti, m'mene ndikadye Paska pamodzi ndi ophunzira anga?


Ndipo m'mene anati ichi anachoka naitana Maria mbale wake m'tseri, ndi kuti, Wafika Mphunzitsi, akuitana iwe.


Inu munditcha Ine Mphunzitsi, ndi Ambuye: ndipo munena bwino; pakuti ndine amene.


Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa