Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 13:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo pamenepo adzatuma angelo, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake ochokera kumphepo zinai, kuyambira ku malekezero ake a dziko lapansi, ndi kufikira ku malekezero a thambo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo pamenepo adzatuma angelo, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake ochokera kumphepo zinai, kuyambira ku malekezero ake a dziko lapansi, ndi kufikira ku malekezero a thambo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Tsono Iye adzatuma angelo ake kuti akasonkhanitse osankhidwa ake kuchokera ku mbali zonse, kuyambira ku malekezero ena a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Ndipo adzatuma angelo ake kukasonkhanitsa osankhidwiratu ake ku mphepo zinayi, kuyambira kumalekezero a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.

Onani mutuwo Koperani




Marko 13:27
27 Mawu Ofanana  

Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.


Ndipo ndidzatulutsa mbeu mwa Yakobo, ndi mwa Yuda wolowa nyumba wa mapiri anga; ndipo osankhidwa anga adzalandira cholowa chao, ndi atumiki anga adzakhala kumeneko.


Haya, haya, thawani kudziko la kumpoto ati Yehova; pakuti ndinakubalalitsani ngati mphepo zinai za kuthambo, ati Yehova.


Mfumu yaikazi ya kumwera adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iye anachokera kumathero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomoni; ndipo onani, wakuposa Solomoni ali pano.


Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusaweruzika,


Padzatero pa chimaliziro cha nthawi ya pansi pano: angelo adzatuluka, nadzawasankhula oipa pakati pa abwino,


Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense: koma chifukwa cha osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.


chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.


Ndipo Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kumphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena.


Ndipo Ambuye akadapanda kufupikitsa masikuwo, sakadapulumuka munthu mmodzi yense; koma chifukwa cha osankhidwa amene anawasankha, anafupikitsa masikuwo.


pakuti adzauka Akhristu onyenga ndi aneneri onyenga, ndipo adzachita zizindikiro ndi zozizwitsa, kuti akasocheretse, ngati nkutheka, osankhidwa omwe.


Ndipo phunzirani ndi mkuyu fanizo lake; pamene pafika kuti nthambi yake ikhala yanthete, ndipo anaphuka masamba ake, muzindikira kuti layandikira dzinja;


Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka kuchifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, naikidwa m'manda.


Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima?


Ndipo nkhosa zina ndili nazo, zimene sizili za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mau anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.


ndipo si chifukwa cha mtunduwo wokha ai, koma kuti akasonkhanitse pamodzi ana a Mulungu akubalalikawo.


Ndani adzaneneza osankhidwa a Mulungu? Mulungu ndiye amene awayesa olungama;


Otayika anu akakhala ku malekezero a thambo, Yehova Mulungu wanu adzakumemezani kumeneko, nadzakutenganiko;


Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;


Ndipo tikupemphani, abale, chifukwa cha kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi kusonkhana pamodzi kwathu kwa Iye;


Mwa ichi ndipirira zonse, chifukwa cha osankhika, kuti iwonso akapeze chipulumutsocho cha mwa Khristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha.


monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo, ndi mtendere zichulukire inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa