Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 11:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo m'mene anapitapo m'mawa mwake, anaona kuti mkuyu uja unafota, kuyambira kumizu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo m'mene anapitapo m'mawa mwake, anaona kuti mkuyu uja unafota, kuyambira kumizu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 M'maŵa mwake, m'mamaŵa ndithu, iwo akuyenda mu mseu, adaona mkuyu uja waumiratu wonse ndi mizu yomwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Mmamawa, pamene ankayenda, anaona mtengo wamkuyu uja utafota kuyambira ku mizu.

Onani mutuwo Koperani




Marko 11:20
14 Mawu Ofanana  

Mizu yake iyangayanga pa kasupe wamadzi, apenyerera pokhalapo miyala.


Inde sanaokedwe, inde sanafesedwe; inde, muzu wao sunazike pansi; koma Iye anawaombetsera mphepo, ndipo afota, ndipo kamvulumvulu awachotsa monga chiputu.


Ndikanachitanso chiyani ndi munda wanga wampesa, chimene sindinachite m'menemo; muja ndinayembekeza kuti udzabala mphesa, wabaliranji mphesa zosadya?


Ndipo m'mene dzuwa linakwera zinapserera; ndipo popeza zinalibe mizu zinafota.


Koma Iye anayankha nati, Mmera wonse, umene Atate wanga wa Kumwamba sanaubzale, udzazulidwa.


Ndipo mamawa, m'mene Iye analinkunkanso kumzinda, anamva njala.


Ndipo m'mawa mwake, atatuluka ku Betaniya, Iye anamva njala.


Ndipo anayankha nanena ndi uwo, Munthu sadzadyanso zipatso zako nthawi zonse. Ndipo ophunzira ake anamva.


Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha.


koma ikabala minga ndi mitungwi, itayika; nitsala pang'ono ikadatembereredwa; chitsiriziro chake ndicho kutenthedwa.


Iwo ndiwo okhala mawanga pa maphwando anu a chikondano, pakudya nanu pamodzi, akudziweta okha opanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofafa kawiri, yozuka mizu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa