Marko 11:2 - Buku Lopatulika2 nanena nao, Mukani, lowani m'mudzi wapandunji ndi inu; ndipo pomwepo pakulowamo mudzapeza mwana wa bulu womangidwa, amene palibe munthu anakhalapo kale lonse; mmasuleni, ndipo mubwere naye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 nanena nao, Mukani, lowani m'mudzi wapandunji ndi inu; ndipo pomwepo pakulowamo mudzapeza mwana wa bulu womangidwa, amene palibe munthu anakhalapo kale lonse; mmasuleni, ndipo mubwere naye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 naŵauza kuti, “Pitani m'mudzi mukuwonawo. Mukangoloŵamo, mukapeza mwanawabulu ali chimangire, amene munthu sanakwerepo chikhalire. Mukammasule nkubwera naye. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 nati kwa iwo, “Pitani ku mudzi uli patsogolo panu, ndipo mukamakalowa, mukapeza mwana wabulu atamangiriridwa pamenepo, amene wina aliyense sanakwerepo. Kamumasuleni ndi kubwera naye kuno. Onani mutuwo |