Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 11:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo anaphunzitsa, nanena nao, Sichilembedwa kodi, Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse? Koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo anaphunzitsa, nanena nao, Sichilembedwa kodi, Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse? Koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Pambuyo pake adayamba kuŵaphunzitsa naŵauza kuti, “Paja Malembo akuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.’ Koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Ndipo pamene ankawaphunzitsa, Iye anati, “Kodi sikunalembedwe kuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero kwa anthu a mitundu yonse?’ Koma inu mwayisandutsa ‘phanga la achifwamba.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Marko 11:17
9 Mawu Ofanana  

naonso ndidzanka nao kuphiri langa lopatulika, ndi kuwasangalatsa m'nyumba yanga yopemphereramo; zopereka zao zopsereza ndi nsembe zao zidzalandiridwa paguwa langa la nsembe; pakuti nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu onse.


Zoweta za Kedara zidzasonkhana kwa iwe, nkhosa zamphongo za Nebayoti zidzakutumikira; izo zidzafika ndi kulandiridwa paguwa langa la nsembe; ndipo ndidzakometsa nyumba ya ulemerero wanga.


Kodi nyumba ino, imene itchedwa dzina langa, ikhala phanga la okwatula pamaso panu? Taona, Ine ndachiona, ati Yehova.


Ndiye Mkanani, m'dzanja lake muli miyeso yonyenga, akonda kusautsa.


ndipo sanalole munthu aliyense kunyamula chotengera kupyola pakati pa Kachisi.


Kwalembedwa, Ndipo nyumba yanga idzakhala nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.


Ndipo anapeza mu Kachisi iwo akugulitsa ng'ombe ndi nkhosa ndi nkhunda, ndi akusinthana ndalama alikukhala pansi.


nati kwa iwo akugulitsa nkhunda, Chotsani izi muno; musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa