Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 10:48 - Buku Lopatulika

48 Ndipo ambiri anamulamula kuti atonthole: koma makamaka anafuulitsa kuti, Inu mwana wa Davide, mundichitire chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

48 Ndipo ambiri anamulamula kuti atonthole: koma makamaka anafuulitsa kuti, Inu mwana wa Davide, mundichitire chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

48 Anthu ambiri adamzazira kuti akhale chete. Koma iye adafuulirafuulira kuti, “Inu Mwana wa Davide, mundichitire chifundo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

48 Ambiri anamukalipira ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulitsabe kuti, “Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”

Onani mutuwo Koperani




Marko 10:48
15 Mawu Ofanana  

Chifundonso ndi chanu, Ambuye, Chifukwa Inu mubwezera munthu aliyense monga mwa ntchito yake.


Ndipo mudzandifuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.


Pamenepo anadza nato tiana kwa Iye, kuti Iye aike manja ake pa ito, ndi kupemphera: koma ophunzirawo anawadzudzula.


Ndipo khamulo linawaletsa, kuti atonthole: koma anakuwitsa, nanena, Ambuye, mutichitire chifundo, Inu Mwana wa Davide.


Ndipo popita Yesu kuchokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, ofuula ndi kuti, Mutichitire ife chifundo, mwana wa Davide.


Ndipo analinkudza nato kwa Iye tiana, kuti akatikhudze; ndipo ophunzirawo anawadzudzula.


M'mene iye ali chilankhulire, anafika a kunyumba ya mkulu wa sunagoge, nanena, kuti, Mwana wako wafa; uvutiranjinso Mphunzitsi?


Ndipo iwo akutsogolera anamdzudzula iye, kuti akhale chete; koma iye anafuulitsa chifuulire, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo.


mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,


Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa