Marko 10:46 - Buku Lopatulika46 Ndipo iwo anafika ku Yeriko; ndipo m'mene Iye analikutuluka mu Yeriko, ndi ophunzira ake, ndi khamu lalikulu la anthu, mwana wa Timeo, Baratimeo, wopempha wakhungu, analikukhala pansi m'mbali mwa njira. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201446 Ndipo iwo anafika ku Yeriko; ndipo m'mene Iye analikutuluka m'Yeriko, ndi ophunzira ake, ndi khamu lalikulu la anthu, mwana wa Timeo, Baratimeo, wopempha wakhungu, analikukhala pansi m'mbali mwa njira. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa46 Yesu ndi ophunzira ake pamodzi ndi gulu lalikulu la anthu adafika ku mzinda wa Yeriko. Tsono pamene ankatuluka mumzindamo, adapeza wakhungu wina wopemphapempha atakhala pansi pamphepete pa mseu. Munthuyo dzina lake anali Baratimeo, mwana wa Timeo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero46 Ndipo anafika ku Yeriko. Pamene Yesu ndi ophunzira ake, pamodzi ndi gulu lalikulu la anthu, ankatuluka mu mzinda, munthu wosaona, Bartumeyu (mwana wa Tumeyu), amakhala mʼmbali mwa msewu ali kupempha. Onani mutuwo |