Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 10:37 - Buku Lopatulika

37 Ndipo iwo anati kwa Iye, Mutipatse ife kuti tikhale mmodzi kudzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, mu ulemerero wanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 Ndipo iwo anati kwa Iye, Mutipatse ife kuti tikhale mmodzi kudzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, m'ulemerero wanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 Iwo adati, “Timafuna kuti pamene mudzakhale mu ulemerero wanu, mudzatiike wina ku dzanja lanu lamanja, wina ku dzanja lanu lamanzere.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 Iwo anayankha kuti, “Timafuna kuti mmodzi wa ife adzakhale kumanja ndi wina kumanzere mu ulemerero wanu.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 10:37
10 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Chifukwa chake tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lili chilili m'mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere.


Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.


Mwa omveka anu muli ana aakazi a mafumu; ku dzanja lanu lamanja aima mkazi wa mfumu wovala golide wa ku Ofiri.


Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m'kubadwanso, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele.


Koma pamene Mwana wa Munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake:


Ndipo Iye anati kwa iwo, Mufuna kuti ndidzakuchitireni inu chiyani?


Pamenepo Ambuye Yesu, atatha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala padzanja lamanja la Mulungu.


Pakuti yense wakuchita manyazi chifukwa cha Ine, ndi cha mau anga mu mbadwo uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachitanso manyazi chifukwa cha iyeyu, pamene Iye adzafika nao angelo ake oyera, mu ulemerero wa Atate wake.


Kodi sanayenere Khristu kumva zowawa izi, ndi kulowa ulemerero wake?


ndi kusanthula nthawi yiti, kapena nthawi yanji Mzimu wa Khristu wokhala mwa iwo analozera, pakuchitiratu umboni wa masautso a Khristu, ndi ulemerero wotsatana nao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa