Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 5:8 - Buku Lopatulika

8 Akapolo atilamulira; palibe wotipulumutsa m'dzanja lao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Akapolo atilamulira; palibe wotipulumutsa m'dzanja lao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Amene akutilamulira ndi akapolo, palibe ndi mmodzi yemwe wotipulumutsa m'manja mwao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Akapolo akutilamulira, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe angatimasule mʼdzanja lawo.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 5:8
12 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Wotembereredwa ndi Kanani; adzakhala kwa abale ake kapolo wa akapolo.


Koma Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapolo Mwamoniyo, ndi Gesemu Mwarabu, anamva natiseka pwepwete, natipeputsa, nati, Chiyani ichi muchichita? Mulikupandukira mfumu kodi?


Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndi siliva masekeli makumi anai; angakhale anyamata ao anachita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, chifukwa cha kuopa Mulungu.


chinkana mudziwa kuti sindili woipa, ndipo palibe wakupulumutsa m'dzanja lanu?


Ana ake akhala otekeseka, napsinjika kuchipata, wopanda wina wakuwapulumutsa.


Dziwitsani ichi inu oiwala Mulungu, kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi.


kuti angamwetule moyo wanga ngati mkango, ndi kuukadzula, wopanda wina wondilanditsa.


chifukwa cha kapolo pamene ali mfumu; ndi chitsiru chitakhuta zakudya;


Inde chiyambire nthawi Ine ndine, ndipo palibe wina wopulumutsa m'dzanja langa; ndidzagwira ntchito, ndipo ndani adzaletsa?


Ndipo tsopano ndidzaonetsa manyazi ake pamaso pa omkonda, popandanso wakumlanditsa m'dzanja langa.


Pakuti sindidzachitiranso chifundo okhala m'dzikomo, ati Yehova; koma taonani, ndidzapereka anthu, yense m'dzanja la mnansi wake, ndi m'dzanja la mfumu yake; ndipo iwo adzakantha dzikoli, ndi m'dzanja mwao sindidzawalanditsa.


Mlendo wokhala pakati panu adzakulirakulira inu, koma inu mudzacheperachepera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa