Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 5:12 - Buku Lopatulika

12 Anawapachika akalonga manja ao; sanalemekeze nkhope za akulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Anawapachika akalonga manja ao; sanalemekeze nkhope za akulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Akalonga akuŵapachika pomangirira manja ao, akuluakulu sakuŵalemekeza konse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Akalonga athu akuwapachika pomangirira manja awo, akuluakulu sakuwalemekeza.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 5:12
8 Mawu Ofanana  

Ndinakwiyira anthu anga, ndinaipitsa cholowa changa, ndi kuwapereka m'manja ako; koma iwe sunawaonetsere chifundo; wasenzetsa okalamba goli lako lolemera ndithu.


Akulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi natonthola; aponya fumbi pa mitu yao, anamangirira chiguduli m'chuuno mwao: Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa pansi mitu yao.


Onani Yehova, nimupenye, mwachitira ayani ichi? Kodi akazi adzadya zipatso zao, kunena ana amene anawalera wokha? Kodi wansembe ndi mneneri adzaphedwa m'malo opatulika a Ambuye?


Mkwiyo wa Yehova unawalekanitsa, sadzawasamaliranso; iwo sanalemekeze ansembe, sanakomere mtima akulu.


Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba; nuope Mulungu wako; Ine ndine Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa