Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 4:13 - Buku Lopatulika

13 Ndicho chifukwa cha machimo a aneneri ndi mphulupulu za ansembe ake, amene anakhetsa mwazi wa olungama pakati pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndicho chifukwa cha machimo a aneneri ndi mphulupulu za ansembe ake, amene anakhetsa mwazi wa olungama pakati pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Zimenezi zidachitika chifukwa cha machimo a aneneri ake ndi ntchito zoipa za ansembe ake, amene ankakhetsa magazi a anthu osalakwa m'malinga amumzindamu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Koma izi zinachitika chifukwa cha kuchimwa kwa aneneri ake ndi mphulupulu za ansembe ake, amene ankapha anthu osalakwa pakati pawo.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 4:13
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa ine, Aneneri anenera zonama m'dzina langa; sindinatume iwo, sindinauze iwo, sindinanene nao; anenera kwa inu masomphenya onama, ndi ula, ndi chinthu chachabe, ndi chinyengo cha mtima wao.


Pakuti kale lomwe ndinathyola goli lako, ndi kudula zomangira zako; ndipo unati, Sindidzakutumikirani, pakuti pa zitunda zonse zazitali, ndi patsinde pa mitengo yonse yaiwisi unawerama, ndi kuchita dama.


Ndapanda ana anu mwachabe; sanamvere kulanga; lupanga lanu ladya aneneri anu, monga mkango wakuononga.


aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?


Pakuti kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu onse akhala akusirira; ndiponso kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita monyenga.


Aneneri ako anakuonera masomphenya achabe ndi opusa; osawulula mphulupulu yako kuti abweze undende wako, koma anakuonera manenero achabe ndi opambutsa.


Mwachulukitsa ophedwa anu m'mzinda muno, mwadzazanso makwalala ake ndi ophedwawo.


Pali chiwembu cha aneneri ake pakati pake, ngati mkango wobangula womwetula nyama, analusira miyoyo, alanda chuma ndi za mtengo wake, achulukitsa amasiye pakati pake.


Pomwepo mutsimikiza nokha, kuti muli ana a iwo amene anapha aneneri.


Ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunze? Ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; wa Iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa