Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 3:7 - Buku Lopatulika

7 Wanditsekereza ndi guta, sindingatuluke; walemeretsa unyolo wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Wanditsekereza ndi guta, sindingatuluke; walemeretsa unyolo wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Adanditsekera m'malinga kuti ndisathaŵe. Adandimanga ndi maunyolo olemera kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Wandimangira khoma kotero kuti sindingathawe, wandimanga ndi maunyolo.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 3:7
11 Mawu Ofanana  

Iye ananditsekera njira kuti ndisapitireko, naika mdima poyendapo ine.


Amuonetseranji kuunika munthu wa njira yobisika, amene wamtsekera Mulungu?


Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali; munandiika ndiwakhalire chonyansa. Ananditsekereza, osakhoza kutuluka ine.


Diso langa lapuwala chifukwa cha kuzunzika kwanga: Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse; nditambalitsira manja anga kwa Inu.


Ndipo anatenga Yeremiya, namponya iye m'dzenje la Malikiya mwana wake wa mfumu, limene linali m'bwalo la kaidi; ndipo anamtsitsa Yeremiya ndi zingwe. Koma m'dzenjemo munalibe madzi, koma thope; namira Yeremiya m'thopemo.


Ndipo tsopano, taona, ndikumasula iwe lero maunyolo ali pa manja ako. Kukakukomera kudza nane ku Babiloni, idza, ndipo ndidzakusamalira bwino; koma kukakuipira kudza nane ku Babiloni, tsala; taona, dziko lonse lili pamaso pako; kulikonse ukuyesa kwabwino kapena koyenera kupitako, pita kumeneko.


Goli la zolakwa zanga lamangidwa ndi dzanja lake; zalukidwa, zakwera pakhosi panga; iye wakhumudwitsa mphamvu yanga; Ambuye wandipereka m'manja mwao, sindithai kuwagonjetsa.


Watsekereza njira zanga ndi miyala yosema, nakhotetsa mayendedwe anga.


Otilondola atigwira pakhosi pathu, tatopa osaona popumira.


Ndipo anakwaniritsa mau ake adanenawo, kutitsutsa ife ndi oweruza athu otiweruza, ndi kutitengera choipa chachikulu; pakuti pansi pa thambo lonse sipanachitike monga umo panachitikira Yerusalemu.


Chifukwa chake taonani, ndidzatchinga njira yako ndi minga, ndipo ndidzammangira mpanda, kuti asapeze mabande ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa