Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 3:51 - Buku Lopatulika

51 Diso langa limvetsa moyo wanga zowawa chifukwa cha ana aakazi onse a m'mzinda mwanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

51 Diso langa limvetsa moyo wanga zowawa chifukwa cha ana akazi onse a m'mudzi mwanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

51 Mtima wanga ukupweteka poona zimene zikuŵachitikira akazi a mumzinda mwanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

51 Mtima wanga ukupweteka poona zimenezi chifukwa cha akazi onse a mu mzinda.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 3:51
14 Mawu Ofanana  

Pakuti ndidzakwera bwanji kwa atate wanga, mnyamatayo akapanda kukhala ndi ine? Ndingaone choipa chidzagwera atate wanga.


chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzalanga iwo; anyamata adzafa ndi lupanga; ana ao aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala;


Ndipo anthu amene adzanenera kwa inu adzaponyedwa kunja m'miseu ya Yerusalemu chifukwa cha chilala ndi lupanga; ndipo adzasowa akuwaika, ndi akazi ao, ndi ana ao aamuna ndi aakazi; ndipo ndidzatsanulira pa iwo zoipa zao.


Ndikatulukira kumunda, taonani ophedwa ndi lupanga! Ndikalowa m'mzinda, taonani odwala ndi njala! Pakuti mneneri ndi wansembe ayendayenda m'dziko osadziwa kanthu.


Ndipo ndidzadyetsa iwo mnofu wa ana ao aamuna ndi aakazi, ndipo adzadya yense mnofu wa mbale wake, m'nkhondo yozinga ndi m'kupsinjikako, kumene adani ao, ndi iwo akufuna moyo wao, adzapsinja iwo nako.


Yehova ali wolungama; pakuti ndapikisana ndi m'kamwa mwake; mumvetu, mitundu ya anthu nonsenu, nimuone chisoni changa; anamwali ndi anyamata anga atha kulowa m'ndende.


Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka; chiwindi changa chagwa pansi chifukwa cha kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga; chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mzindawu.


Wamng'ono ndi nkhalamba agona pansi m'makwalala; anamwali ndi anyamata anga agwa ndi lupanga; munawapha tsiku la mkwiyo wanu, munawagwaza osachitira chisoni.


kufikira Yehova adzazolika kumwamba ndi kuona.


Ondida opanda chifukwa anandiinga ngati mbalame;


Anaipitsa akazi mu Ziyoni, ndi anamwali m'midzi ya Yuda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa