Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 3:5 - Buku Lopatulika

5 Wandimangira zithando za nkhondo, wandizinga ndi ulembe ndi mavuto.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Wandimangira zithando za nkhondo, wandizinga ndi ulembe ndi mavuto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Adandizinga ndi kundizunguliza ponseponse ndi mazunzo ndi masautso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Wandizinga ndi kundizungulira ndi zowawa ndi zolemetsa.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 3:5
8 Mawu Ofanana  

Iye ananditsekera njira kuti ndisapitireko, naika mdima poyendapo ine.


Ndipo anandipatsa ndulu ikhale chakudya changa; nandimwetsa vinyo wosasa pomva ludzu ine.


Chifukwa chake Yehova wa makamu atero za aneneri: Taonani, ndidzadyetsa iwo chowawa, ndidzamwetsa iwo madzi andulu; pakuti kwa aneneri a ku Yerusalemu kuipitsa kwatulukira kunka ku dziko lonse.


Tikhaliranji ife? Tasonkhanani, tilowe m'mizinda yamalinga, tikhale chete m'menemo; pakuti Yehova Mulungu wathu watikhalitsa ife chete, natipatsa ife madzi a ndulu timwe, pakuti tamchimwira Yehova.


chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Taonani, ndidzadyetsa anthu awa chivumulo, ndi kuwamwetsa madzi andulu.


Kumbukirani msauko wanga ndi kusochera kwanga, ndizo chivumulo ndi ndulu.


Koma pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipulumutso chake chayandikira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa