Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 3:1 - Buku Lopatulika

1 Ine ndine munthuyu wakuona msauko ndi ndodo ya ukali wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ine ndine munthuyu wakuona msauko ndi ndodo ya ukali wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ine ndine munthu amene ndaona mavuto, ndalangidwa ndi ndodo ya ukali wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ine ndine munthu amene ndaona masautso ndi ndodo ya ukali wake.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 3:1
12 Mawu Ofanana  

Ndichitireni chifundo, ndichitireni chifundo, mabwenzi anga inu; pakuti dzanja la Mulungu landikhudza.


Masiku anga akunga mthunzi womka m'tali; ndipo ine ndauma ngati udzu.


Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa, mudzatipatsanso moyo, ndi kutitenganso munsi mwa dziko.


Mkwiyo wanu utsamira pa ine, ndipo munandizunza ine ndi mafunde anu onse.


Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.


Ndipo anatenga Yeremiya, namponya iye m'dzenje la Malikiya mwana wake wa mfumu, limene linali m'bwalo la kaidi; ndipo anamtsitsa Yeremiya ndi zingwe. Koma m'dzenjemo munalibe madzi, koma thope; namira Yeremiya m'thopemo.


ndi amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi ana aakazi a mfumu, ndi anthu onse amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya ndi Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, mwana wake wa Safani, ndi Yeremiya mneneri, ndi Baruki mwana wake wa Neriya;


Bala la mwana wamkazi wa anthu anga ndaphwetekwa nalo; ndada mtima; kudabwa kwandigwira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa