Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 2:7 - Buku Lopatulika

7 Ambuye wataya guwa lake la nsembe, malo ake opatulika amnyansira; wapereka m'manja a adani ake makoma a zinyumba zake; iwo anapokosera m'nyumba ya Yehova ngati tsiku la msonkhano.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ambuye wataya guwa lake la nsembe, malo ake opatulika amnyansira; wapereka m'manja a adani ake makoma a zinyumba zake; iwo anaphokosera m'nyumba ya Yehova ngati tsiku la msonkhano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Chauta adanyoza ngakhale guwa lake lomwe, ndipo adaŵakana malo ake opatulika. Adapereka malinga a nyumba zake zachifumu m'manja mwa adani ake. M'nyumba yeniyeni ya Chauta adaniwo adafuula ndi chimwemwe monga momwe zimachitikira pa tsiku lachikondwerero.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ambuye wakana guwa lake la nsembe ndipo wasiya malo ake opatulika. Iye wapereka makoma a nyumba zake zaufumu kwa mdani wake; adaniwo anafuwula mʼnyumba ya Yehova ngati kuti ndi pa tsiku la chikondwerero.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 2:7
31 Mawu Ofanana  

natentha nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu; ndi nyumba zonse zazikulu anazitentha ndi moto.


Ndipo anatentha nyumba ya Mulungu, nagumula linga la Yerusalemu, natentha nyumba zake zonse zachifumu ndi moto, naononga zipangizo zake zonse zokoma.


Munakaniza chipangano cha mtumiki wanu; munaipsa korona wake ndi kumponya pansi.


Musakwiye kopambana, Yehova, musakumbukire zoipa nthawi zonse; taonani, yang'anani ife, tikupembedzani Inu, ife tonse tili anthu anu.


Yehova, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzabweza zida za nkhondo zimene zili m'manja anu, zimene mumenyana nazo ndi mfumu ya ku Babiloni, ndi Ababiloni akuzinga inu, kunja kwa malinga, ndipo ndidzazisonkhanitsa pakati pa mzinda uwu.


Mika Mmoreseti ananenera masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda; ndipo iye ananena kwa anthu onse a Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero: Ziyoni adzalimidwa ngati munda, Yerusalemu adzakhala miunda, ndi phiri la nyumba longa misanje ya nkhalango.


pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mzinda uwu chitemberero cha kwa mitundu yonse ya dziko lapansi.


ndipo Ababiloni, olimbana ndi mzinda uwu, adzafika nadzayatsa mzindawu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukizira Baala, pa machitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu ina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga.


Ndipo Ababiloni anatentha ndi moto nyumba ya mfumu, ndi nyumba za anthu, nagumula malinga a Yerusalemu.


Ndinaona, ndipo taona, munda wazipatso unali chipululu, ndipo mizinda yake yonse inapasuka pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa mkwiyo wake woopsa.


Pakuti Yehova atero, Dziko lonse lidzakhala bwinja koma sindidzatsirizitsa.


Mau a iwo akuthawa akupulumuka m'dziko la Babiloni, kuti alalikire mu Ziyoni kubwezera chilango kwa Yehova Mulungu wathu, kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake.


ndipo anatentha nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu, ngakhale zinyumba zazikulu zonse, anazitentha ndi moto.


M'njira za Ziyoni mulira posoweka akudzera msonkhano; pa zipata zake zonse papasuka; ansembe ake onse ausa moyo; anamwali ake asautsidwa; iye mwini namva zowawa.


Ambuye waphimbatu ndi mtambo mwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira! Wagwetsa pansi kuchokera kumwamba kukoma kwake kwa Israele; osakumbukira poponda mapazi ake tsiku la mkwiyo wake.


Ambuye wasanduka mdani, wameza Israele; wameza zinyumba zake zonse, wapasula malinga ake; nachulukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi chibumo.


Nena ndi nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzadetsa malo anga opatulika, ulemerero wa mphamvu yanu, chokonda m'maso mwanu, chimene moyo wanu ali nacho chifundo; ndipo ana anu aamuna ndi aakazi otsalira inu adzagwa ndi lupanga.


Chifukwa chake ndidzabwera nao amitundu oipitsitsa, ndipo iwo adzalandira nyumba zao ngati cholowa, ndidzaleketsanso kudzikuza kwa amphamvu, kuti adetsedwe malo ao opatulika.


Ndipo ndidzasandutsa mizinda yanu bwinja, ndi kupasula malo anu opatulika, wosanunkhiza Ine za fungo lanu lokoma.


Ndiponso pali ichinso: pokhala iwo m'dziko la adani ao sindidzawakaniza, kapena kunyansidwa nao, kuwaononga konse, ndi kuthyola pangano langa ndinapangana nao; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wao.


koma ndidzatumiza moto pa Yuda, udzanyeketsa nyumba zachifumu za mu Yerusalemu.


Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi mu Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango.


Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Simuona izi zonse kodi? Indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzake, umene sudzagwetsedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa