Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 2:18 - Buku Lopatulika

18 Mtima wao unafuula kwa Ambuye, linga iwe la mwana wamkazi wa Ziyoni, igwe misozi ngati mtsinje usana ndi usiku; usapume kanthawi, asaleke mwana wa diso lako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Mtima wao unafuula kwa Ambuye, linga iwe la mwana wamkazi wa Ziyoni, igwe misozi ngati mtsinje usana ndi usiku; usapume kanthawi, asaleke mwana wa diso lako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Fuulani kwamphamvu kwa Ambuye, inu anthu a ku Ziyoni. Misozi yanu ichite kuti yoyoyo, ngati mtsinje, usana ndi usiku. Musadzipatse nthaŵi yoti mupumule. Misozi yanu isalekeze.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Mitima ya anthu ikufuwulira Ambuye. Iwe khoma la mwana wamkazi wa Ziyoni, misozi yako itsike ngati mtsinje usana ndi usiku; usadzipatse wekha mpumulo, maso ako asaleke kukhetsa misozi.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 2:18
14 Mawu Ofanana  

Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi, popeza sasamalira chilamulo chanu.


Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova; ndidzasunga malemba anu.


Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri chifukwa cha kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, chifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga.


Ndipo udzati kwa iwo mau awa, Maso anga agwe misozi usana ndi usiku, asaleke; pakuti namwali mwana wa anthu anga wasweka ndi kusweka kwakukulu, ndi bala lopweteka kwambiri.


Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wake woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ake, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! Pakuti moyo wanga walefuka chifukwa cha ambanda.


Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!


Chifukwa cha zimenezi ndilira; diso langa, diso langatu likudza madzi: Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditalikira; ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana.


Uliralira usiku; misozi yake ili pa masaya ake; mwa onse amene anaukonda mulibe mmodzi wakuutonthoza: Mabwenzi ake onse auchitira ziwembu, asanduka adani ake.


Yehova watsimikiza mtima kupasula linga la mwana wamkazi wa Ziyoni; watambalika chingwe, osabweza dzanja lake kuti lisaonongepo; waliritsa tchemba ndi linga; zilefuka pamodzi.


Ndipo sanafuulire kwa Ine ndi mtima wao, koma alira pakama pao, asonkhanira tirigu ndi vinyo, apikisana ndi Ine.


Pakuti mwala wa m'khoma ufuula, ndi mtanda wa kuphaso udzauvomereza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa