Maliro 2:16 - Buku Lopatulika16 Adani ako onse ayasamira pa iwe, atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza; ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Adani ako onse ayasamira pa iwe, atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza; ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Adani ako onse akukuyasamira kukamwa mwaukali, ndipo akukunyodola. Akukutsonya ndi kumakukuta mano ao namanena kuti, “Tafikapodi pousakaza! Ah! Tsiku lija tinkafunali ndi lero. Tagonera, taliwonadi.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Adani ako onse akutsekulira pakamwa ndi kukunyoza; iwo akunyogodola ndi kukukuta mano awo, ndipo akuti, “Tamumeza. Tsiku ili ndi lomwe timayembekezera; tili ndi moyo kuti tilione.” Onani mutuwo |