Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 2:13 - Buku Lopatulika

13 Ndikuchitire umboni wotani? Ndikuyerekeze ndi chiyani, mwana wamkazi wa Yerusalemu? Ndikulinganize ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni? Popeza akula ngati nyanja; ndani angakuchize?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndikuchitire umboni wotani? Ndikuyerekeze ndi chiyani, mwana wamkazi wa Yerusalemu? Ndikulinganize ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni? Popeza akula ngati nyanja; ndani angakuchize?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Iwe mzinda wa Yerusalemu, ndinganene chiyani za iwe, kaya nkukuyerekeza ndi chiyani? Iwe mzinda wangwiro wa Ziyoni, kodi ndingakufanizire ndi yani, kuti choncho ndikusangalatse? Kuwonongeka kwako nkwakukulu ngati nyanja. Ndani angathe kukukonzanso?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ndinganene chiyani za iwe? Ndingakufanizire ndi chiyani, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu? Kodi ndingakufanizire ndi yani kuti ndikutonthoze, iwe namwali wa Ziyoni? Chilonda chako ndi chozama ngati nyanja, kodi ndani angakuchiritse?

Onani mutuwo Koperani




Maliro 2:13
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anafika ku Baala-Perazimu, nawakantha kumeneko Davideyo; nati, Yehova wathyola adani anga pamaso panga ngati madzi okamulira. Chifukwa chake analitcha dzina la malowo Baala-Perazimu.


Mau a Yehova akumnenera iye ndi awa, Namwali mwana wamkazi wa Ziyoni akunyoza, akuseka mwana wamkazi wa Yerusalemu, akupukusira mutu pambuyo pako.


Mwagwedeza dziko, mwaling'amba. Konzani ming'alu yake; pakuti ligwedezeka.


awa ndiwo mau amene Yehova wanena za iye, Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza iwe ndi kuseka iwe ndi chiphwete; mwana wamkazi wa Yerusalemu wapukusa mutu wake pambuyo pako.


Ndipo udzati kwa iwo mau awa, Maso anga agwe misozi usana ndi usiku, asaleke; pakuti namwali mwana wa anthu anga wasweka ndi kusweka kwakukulu, ndi bala lopweteka kwambiri.


Kodi mwakanadi Yuda? Kodi mtima wanu wanyansidwa ndi Ziyoni? Bwanji mwatipanda ife, ndipo tilibe kuchira? Tinayembekeza mtendere, koma sizinafike zabwino; tinayembekeza nthawi yakuchira, ndipo taonani mantha!


Kodi mulibe vunguti mu Giliyadi? Kodi mulibe sing'anga m'menemo; analekeranji kuchira mwana wamkazi wa anthu anga?


afulumire, atikwezere ife mau a maliro, kuti maso athu agwe misozi, ndi zikope zathu ziyendetse madzi.


Kodi muyesa chimenechi chabe, nonsenu opita panjira? Penyani nimuone, kodi chilipo chisoni china ngati changachi amandimvetsa ine, chimene Yehova wandisautsa nacho tsiku la mkwiyo wake waukali?


Farao adzawaona, nadzasangalala nao aunyinji ake onse, Farao ndi ankhondo ake onse ophedwa ndi lupanga, ati Ambuye Yehova.


Ndipo anakwaniritsa mau ake adanenawo, kutitsutsa ife ndi oweruza athu otiweruza, ndi kutitengera choipa chachikulu; pakuti pansi pa thambo lonse sipanachitike monga umo panachitikira Yerusalemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa