Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 2:12 - Buku Lopatulika

12 Amati kwa amao, Tirigu ndi vinyo ali kuti? Pokomoka iwo ngati olasidwa m'makwalala a mzindawu, potsanulidwa miyoyo yao pa zifuwa za amao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Amati kwa amao, Tirigu ndi vinyo ali kuti? Pokomoka iwo ngati olasidwa m'makwalala a mudziwu, potsanulidwa miyoyo yao pa zifuwa za amao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Anawo akufunsa amai ao kuti, “Kodi chakudya ndi chakumwa tingazipeze kuti?” Akufunsa zimenezi pamene akukomoka m'miseu yamumzinda ngati anthu olasidwa. Akuthatha ndi moyo pa mfukato wa amai ao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Anawo akufunsa amayi awo kuti, “Kodi tirigu ndi vinyo zili kuti?” pamene akukomoka ngati anthu olasidwa mʼmisewu ya mʼmizinda, pamene miyoyo yawo ikufowoka mʼmanja mwa amayi awo.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 2:12
9 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano moyo wanga udzitsanulira m'kati mwanga; masiku akuzunza andigwira.


Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine, pakuti ndinkapita ndi unyinji wa anthu, ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu, ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika, ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.


Khulupirirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu, tsanulirani mitima yanu pamaso pake. Mulungu ndiye pothawirapo ife.


Ana ako aamuna akomoka; agona pamutu pa makwalala onse, monga nswala muukonde; adzala ndi ukali wa Yehova, kudzudzula kwa Mulungu wako.


Chifukwa chake ndidzamgawira gawo ndi akulu; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wake kuimfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula machimo a ambiri, napembedzera olakwa.


Adzadya zokolola zako, ndi mkate wako, umene ana ako aamuna ndi aakazi ayenera kudya; adzadya nkhosa zako ndi zoweta zako; adzadya mphesa zako ndi nkhuyu zako; adzapasula ndi lupanga mizinda yamalinga yako, imene ukhulupiriramo.


Anthu ake onse ausa moyo nafunafuna mkate; ndi zokondweretsa zao agula zakudya kuti atsitsimutse moyo wao; taonani, Yehova, nimupenye; pakuti ndasanduka wonyansa.


Lilime la mwana woyamwa limamatira kumalakalaka kwake ndi ludzu; ana aang'ono apempha mkate koma palibe wakuwanyemera.


Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, ndi kuika lupanga langa m'dzanja lake; koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuula pamaso pake mabuulo a munthu wopyozedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa